Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza, wakupanga chovuta chikhale lamulo?
Danieli 2:13 - Buku Lopatulika M'mwemo chilamulirocho chidamveka, ndi eni nzeru adati aphedwe; anafunafunanso Daniele ndi anzake aphedwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 M'mwemo chilamulirocho chidamveka, ndi eni nzeru adati aphedwe; anafunafunanso Daniele ndi anzake aphedwe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho lamulo linaperekedwa kuti anthu anzeru aphedwe, ndipo anatuma anthu kukafunafuna Danieli ndi anzake kuti iwonso aphedwe. |
Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza, wakupanga chovuta chikhale lamulo?
Potero Daniele analowa kwa Ariyoki amene mfumu idamuika aononge eni nzeru a ku Babiloni; anamuka, natero naye, Usaononga eni nzeru a ku Babiloni, undilowetse kwa mfumu, ndipo ndidzaululira mfumu kumasulirako.
ndipo chifukwa cha ukulu adampatsawo anthu onse, mitundu yonse ya anthu, amanenedwe onse, ananjenjemera, naopa pamaso pake; amene anafuna kuwapha anawapha; amene anafuna kuwasunga anawasunga amoyo; amene anafuna kuwakweza anawakweza; amene anafuna kuwatsitsa anawatsitsa.