Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 2:14 - Buku Lopatulika

14 Pamenepo Daniele anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, adatulukawo kukapha eni nzeru a ku Babiloni;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Pamenepo Daniele anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, adatulukawo kukapha eni nzeru a ku Babiloni;

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Danieli anayankhula mwanzeru ndi mwaulemu kwa Ariyoki, mkulu wa asilikali olondera mfumu amene anatumidwa kukapha anthu anzeru a ku Babuloni.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 2:14
8 Mawu Ofanana  

Amidiyani ndipo anamgulitsa iye anke ku Ejipito kwa Potifara, nduna ya Farao, kazembe wa alonda.


Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mzinda, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babiloni.


Mwezi wachisanu, tsiku lakhumi la mwezi, ndicho chaka chakhumi ndi chisanu ndi chinai cha Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, analowa mu Yerusalemu Nebuzaradani kapitao wa alonda, amene anaimirira pamaso pa mfumu ya ku Babiloni:


Ndipo nkhondo yonse ya Ababiloni, imene inali ndi kapitao wa alonda, inagumula makoma onse a Yerusalemu pomzungulira pake.


anayankha nati kwa Ariyoki mkulu wa olindirira a mfumu, Chilamuliro cha mfumu chifulumiriranji? Pamenepo Ariyoki anadziwitsa Daniele chinthuchi.


Potero Daniele analowa kwa Ariyoki amene mfumu idamuika aononge eni nzeru a ku Babiloni; anamuka, natero naye, Usaononga eni nzeru a ku Babiloni, undilowetse kwa mfumu, ndipo ndidzaululira mfumu kumasulirako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa