Ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa m'chuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpso zake.
Danieli 10:5 - Buku Lopatulika ndinakweza maso anga, ndinapenya ndi kuona munthu wovala bafuta, womanga m'chuuno ndi golide woona wa ku Ufazi; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndinakweza maso anga, ndinapenya ndi kuona munthu wovala bafuta, womanga m'chuuno ndi golide woona wa ku Ufazi; Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndinakweza maso ndipo ndinaona kuti pafupi ndi ine panali munthu wochokera ku Ufazi atavala zovala zosalala ndi lamba wa golide woyengeka bwino mʼchiwuno mwake. |
Ndipo chilungamo chidzakhala mpango wa m'chuuno mwake, ndi chikhulupiriko chidzakhala mpango wa pa zimpso zake.
Abwera ndi siliva wa ku Tarisisi, wosulasula wopyapyala ndi golide wa ku Ufazi, ntchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zovala zao ndi nsalu ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi ntchito za muomba.
Ndipo taonani, anadza amuna asanu ndi mmodzi, odzera njira ya chipata cha kumtunda choloza kumpoto, aliyense ndi chida chake chophera m'dzanja lake; ndi munthu mmodzi pakati pao wovala bafuta, ndi zolembera nazo m'chuuno mwake. Ndipo analowa, naima m'mphepete mwa guwa la nsembe lamkuwa.
Ndinaona usiku, taonani, munthu woyenda pa kavalo wofiira, alikuima pakati pa mitengo yamchisu inali kunsi; ndi pambuyo pake panali akavalo ofiira, odera ndi oyera.
Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo;
Ndipo kunali, pokhala Yoswa ku Yeriko, anakweza maso ake, napenya, ndipo taona, panaima munthu pandunji pake ndi lupanga lake losolola m'dzanja lake; namuka Yoswa kuli iye, nati iye, Uvomerezana ndi ife kapena ndi adani athu?