Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Amosi 4:3 - Buku Lopatulika

Ndipo mudzatulukira popasuka linga, yense m'tsogolo mwake, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mudzatulukira popasuka linga, yense m'tsogolo mwake, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mudzatulukira m'ming'alu ya malinga, aliyense payekhapayekha ndipo adzakutayani ku phiri la Halimoni.” Akuterotu Chauta.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mudzatulukira mʼmingʼalu ya pa khoma aliyense payekhapayekha, ndipo mudzatayidwa ku Harimoni,” akutero Yehova.

Onani mutuwo



Amosi 4:3
12 Mawu Ofanana  

Pamenepo linga la mzindawo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku chipata cha pakati pa makoma awiri, ili ku munda wa mfumu; Ababiloni tsono anali pamzinda pouzinga; nimuka mfumu panjira ya kuchidikha.


Ndipo anawalondola mpaka ku Yordani; ndipo taonani, m'njira monse munadzala ndi zovala ndi akatundu adazitaya Aaramu m'kufulumira kwao. Nibwera mithenga, nifotokozera mfumu.


Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze;


Pakuti tsiku limenelo iwo adzataya munthu yense mafano ake asiliva, ndi mafano ake agolide amene manja anuanu anawapanga akuchimwitseni inu.


Pamenepo anaboola mzinda, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, natuluka m'mzinda usiku panjira ya kuchipata cha pakati pa makoma awiri, imene inali pamunda wa mfumu; Ababiloni alikumenyana ndi mzinda pozungulira pake, ndipo anapita njira ya kuchidikha.


Kalongayo ali pakati pao adzasenza paphewa pake mumdima, nadzatuluka; adzaboola palinga, nadzatulutsapo; adzaphimba nkhope yake kuti asapenye dziko ndi maso ake.


Udziboolere khoma pamaso pao, nuwatulutsire akatundu pamenepo.


Chifukwa chake tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita.


Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.


Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?


Giliyadi anakhala tsidya lija la Yordani; ndi Dani, akhaliranji m'zombo? Asere anakhala pansi m'mphepete mwa nyanja, nakhalitsa pa nyondo yake ya nyanja.