Yeremiya 52:7 - Buku Lopatulika7 Pamenepo anaboola mzinda, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, natuluka m'mzinda usiku panjira ya kuchipata cha pakati pa makoma awiri, imene inali pamunda wa mfumu; Ababiloni alikumenyana ndi mzinda pozungulira pake, ndipo anapita njira ya kuchidikha. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Pamenepo anaboola mudzi, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, natuluka m'mudzi usiku pa njira ya kuchipata cha pakati pa makoma awiri, imene inali pa munda wa mfumu; Ababiloni alikumenyana ndi mudzi pozungulira pake, ndipo anapita njira ya kuchidikha. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 malinga a mzindawo adabooledwa. Pamenepo ankhondo onse adathaŵa mumzindamo usiku, kutulukira pa chipata cha pakati pa makoma aŵiri, pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababiloni anali atauzinga mzindawo. Ndipo adathaŵira ku Araba. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Tsono linga la mzindawo linabowoledwa, ndipo ankhondo onse anathawa. Iwo anatuluka mu mzindamo usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri a pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Ndipo anathawira ku Araba, Onani mutuwo |