Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 4:4 - Buku Lopatulika

4 Idzani ku Betele, mudzalakwe ku Giligala, nimuchulukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatuatatu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Idzani ku Betele, mudzalakwe ku Giligala, nimuchulukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatuatatu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 “Bwerani ku malo oyera ku Betele, mudzachimwireko. Bweranazoni nsembe zanu m'maŵa mulimonse, bweranazoni zopereka zanu zachikhumi pa masiku atatu aliwonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Bwerani ku Beteli mudzachimwe; ndi ku Giligala kuti mudzapitirize kuchimwa. Bweretsani nsembe zanu mmawa uliwonse, bweretsani chakhumi chanu masiku atatu aliwonse.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 4:4
16 Mawu Ofanana  

Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.


Ndipo inu, nyumba ya Israele, atero Ambuye Yehova, mukani, tumikirani yense mafano ake, ndi m'tsogolo momwe, popeza simundimvere Ine; koma musaipsanso dzina langa lopatulika ndi zopereka zanu ndi mafano anu.


Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; mu Giligala aphera nsembe ya ng'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'michera ya munda.


Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.


Choipa chao chonse chili mu Giligala; pakuti pamenepo ndinawada, chifukwa cha kuipa kwa machitidwe ao ndidzawainga kuwachotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.


Pakuti tsiku lakumlanga Israele chifukwa cha zolakwa zake, ndidzalanganso maguwa a nsembe a ku Betele; ndi nyanga za guwa la nsembe zidzadulidwa, ndipo zidzagwa pansi.


koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.


Dzazani inu muyeso wa makolo anu.


Pomwepo anadza kwa ophunzira, nanena kwa iwo, Gonani nthawi yatsalayi, mupumule; onani, nthawi yafika, ndipo Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a ochimwa.


Ndipo anadza kachitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; chakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa Munthu aperekedwa m'manja a anthu ochimwa.


Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, anakhala m'manda ndi m'mapiri, nafuula, nadzitematema ndi miyala.


Mutatha kugawa magawo khumi, zobala zanu zonse chaka chachitatu, ndicho chaka chogawa magawo khumi, muzizipereka kwa Mlevi, kwa mlendo, kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, kuti adye m'midzi mwanu, ndi kukhuta.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa