Afilipi 3:21 - Buku Lopatulika amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Iyeyo adzasandutsa matupi athu achabeŵa kuti akhale ofanafana ndi thupi lake laulemerero. Adzachita zimenezi ndi mphamvu zake zomwe zija zimene angathenso kugonjetsa nazo zinthu zonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iyeyo, ndi mphamvu imene imamuthandiza kukhazikitsa zinthu zonse pansi pa ulamuliro wake, adzasintha matupi athu achabewa kuti akhale ofanana ndi thupi lake la ulemerero. |
Iye wameza imfa kunthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa padziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.
Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.
Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.
ndipo Iye anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuwala.
Koma Yesu anayankha, nati kwa iwo, Mungolakwa osadziwa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.
Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.
Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;
Pamene Khristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi Iye mu ulemerero.
Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.
Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.