Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Hoseya 13:14 - Buku Lopatulika

14 Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndidzawaombola kumphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako ili kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Kodi ngati ndidzaŵapulumutsa kwa akufa? Kodi ngati ndidzaŵaombola ku imfa? Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti? Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti? Anthu ameneŵa sindidzaŵachitiranso chifundo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Ndidzawapulumutsa ku mphamvu ya manda; ndidzawawombola ku imfa. Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti? Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti? “Sindidzachitanso chifundo,

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 13:14
32 Mawu Ofanana  

pamenepo Mulungu amchitira chifundo, nati, Mlanditse, angatsikire kumanda, Ndampezera dipo.


Kukhosi kwake kukhala mphamvu, ndi mantha avumbuluka patsogolo pake.


Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.


Yehova munabweza moyo wanga kumanda, munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje.


Koma Mulungu adzaombola moyo wanga kumphamvu ya manda. Pakuti adzandilandira ine.


Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake;


Inu, amene munationetsa nsautso zambiri ndi zoipa, mudzatipatsanso moyo, ndi kutitenganso munsi mwa dziko.


Pakuti chifundo chanu cha pa ine nchachikulu; ndipo munalanditsa moyo wanga kunsi kwa manda.


Iye wameza imfa kunthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa padziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.


Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.


Iwe wandikana Ine, ati Yehova, wabwerera m'mbuyo; chifukwa chake ndatambasulira dzanja langa pa iwe, ndi kukuononga iwe; ndatopa ndi kulekerera.


Munthuyo akhale ngati mizinda imene Yehova anapasula, osalekerera; amve mfuu mamawa, ndi mkuwo pausana;


Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ake agavira; Yehova wa makamu ndi dzina lake:


Ndipo anati kwa ine, Nenera kwa mpweya, nenera, wobadwa ndi munthu iwe, nuti kwa mpweya, Atero Ambuye Yehova, Idza, mpweya iwe, kuchokera kumphepo zinai, nuuzire ophedwa awa, kuti akhale ndi moyo.


Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake.


Ndipo kudzikuza kwa Israele kumchitira umboni pamaso pake; koma sanabwerere kunka kwa Yehova Mulungu wao, kapena kumfunafuna mwa ichi chonse.


Pakuti Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwe.


Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?


Pakuti ngati kuwataya kwao kuli kuyanjanitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwao kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakuchokera kwa akufa?


Pakuti mphatso zake ndi kuitana kwake kwa Mulungu sizilapika.


Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.


amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.


Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu.


Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.


Ndipo nyanja inapereka akufawo anali momwemo, ndipo imfa ndi dziko la akufa zinapereka akufawo anali m'menemo; ndipo anaweruzidwa yense monga mwa ntchito zake.


ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.


Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo dziko la akufa linatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zilombo za padziko.


Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa