Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene munaperekedweracho;
Afilipi 1:3 - Buku Lopatulika Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira inu. |
Koma ayamikidwe Mulungu, kuti ngakhale mudakhala akapolo a uchimo, tsopano mwamvera ndi mtima makhalidwe aja a chiphunzitso chimene munaperekedweracho;
Ndiyamika Mulungu wanga nthawi yonse kaamba ka inu, chifukwa cha chisomo cha Mulungu chinapatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu;
Pakuti tikhoza kubwezera kwa Mulungu chiyamiko chanji chifukwa cha inu, pa chimwemwe chonse tikondwera nacho mwa inu pamaso pa Mulungu wathu;
Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;
Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi chikumbumtima choyera, kuti ndikumbukira iwe kosalekeza m'mapemphero anga,