Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululire ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba.
Afilipi 1:29 - Buku Lopatulika kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu chifukwa cha Khristu, si kukhulupirira kwa Iye kokha, komatunso kumva zowawa chifukwa cha Iye, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu chifukwa cha Khristu, si kukhulupirira kwa Iye kokha, komatunso kumva zowawa chifukwa cha Iye, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja Iye adakupatsani mwai, osati wakungokhulupirira Khristu ai, komanso wakumva zoŵaŵa chifukwa cha Iye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti inu mwapatsidwa mwayi osati ongokhulupirira Khristu kokha, koma wakumva zowawa mʼmalo mwa Khristu. |
Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululire ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba.
ndipo mwa Iye yense wokhulupirira ayesedwa wolungama kumchotsera zonse zimene simunangathe kudzichotsera poyesedwa wolungama ndi chilamulo cha Mose.
nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.
Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.
Pamenepo ndipo anapita kuchokera kubwalo la akulu a milandu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.
Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu;
popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m'chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.
koma popeza mulawana ndi Khristu zowawa zake, kondwerani: kutinso pa vumbulutso la ulemerero wake mukakondwere kwakukulukulu.