Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;
Afilipi 1:21 - Buku Lopatulika Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Khristu, ndi kufa kuli kupindula. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Khristu, ndi kufa kuli kupindula. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kwa inetu moyo ndi Khristu amene, ndipo nayonso imfa ili ndi phindu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti kwa ine kukhala moyo ndi Khristu ndipo kufa ndi phindu. |
Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;
ngati Paulo, kapena Apolo, kapena Kefa, kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena za makono ano, kapena zilinkudza; zonse ndi zanu;
Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.
Pokhala nako kulimbika mtima nthawi zonse tsono, ndipo podziwa kuti pamene tili kwathu m'thupi, sitili kwa Ambuye.
koma tilimbika mtima, ndipo tikondwera makamaka kusakhala m'thupi, ndi kukhala kwathu kwa Ambuye.
Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi.
monga mwa kulingiriritsa ndi chiyembekezo changa, kuti palibe chinthu chidzandichititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Khristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwa moyo, kapena mwa imfa.
Koma ngati kukhala ndi moyo m'thupi ndiko chipatso cha ntchito yanga, sindizindikiranso chimene ndidzasankha.
Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala nacho cholakalaka cha kuchoka kukhala ndi Khristu, ndiko kwabwino koposaposatu;
Pamene Khristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi Iye mu ulemerero.
Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.