Ndipo iye anati, Mtendere ukhale ndi inu, musaope; Mulungu wanu ndi Mulungu wa atate wanu anakupatsani inu chuma m'matumba anu; ine ndinali nazo ndalama zanu. Pamenepo anawatulutsira Simeoni.
3 Yohane 1:14 - Buku Lopatulika koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 koma ndiyembekeza kukuona iwe msanga, ndipo tidzalankhula popenyana. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikuyembekeza kudzakuwona posachedwa. Pamenepo tidzakambirana pakamwa mpakamwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndiyembekezera kufika kwanuko posachedwapa, ndipo tidzakambirana pamaso ndi pamaso. |
Ndipo iye anati, Mtendere ukhale ndi inu, musaope; Mulungu wanu ndi Mulungu wa atate wanu anakupatsani inu chuma m'matumba anu; ine ndinali nazo ndalama zanu. Pamenepo anawatulutsira Simeoni.
Mfumu Nebukadinezara, kwa anthu mitundu ya anthu, ndi a manenedwe okhala padziko lonse lapansi: Mtendere uchulukire inu.
Iyeyu, wapakhomo amtsegulira ndi nkhosa zimva mau ake; ndipo aitana nkhosa za iye yekha maina ao, nazitsogolera kunja.
Pamenepo, pokhala madzulo, tsiku lomwelo, loyamba la Sabata, makomo ali chitsekere, kumene anakhala ophunzira, chifukwa cha kuopa Ayuda, Yesu anadza naimirira pakati pao, nanena nao, Mtendere ukhale ndi inu.
Chifukwa chake Yesu anatinso kwa iwo, Mtendere ukhale ndi inu; monga Atate wandituma Ine, Inenso ndituma inu.
Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu.
Mupatsane moni ndi kupsompsonana kwa chikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Khristu.
Pokhala ndili nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti chimwemwe chanu chikwanire.