Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzachita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu.
2 Samueli 9:12 - Buku Lopatulika Ndipo Mefiboseti anali ndi mwana wamwamuna wamng'ono, dzina lake ndiye Mika. Ndipo onse akukhala m'nyumba ya Ziba anali anyamata a Mefiboseti. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mefiboseti anali ndi mwana wamwamuna wamng'ono, dzina lake ndiye Mika. Ndipo onse akukhala m'nyumba ya Ziba anali anyamata a Mefiboseti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mefiboseti anali ndi mwana wamng'ono, dzina lake Mika. Ndipo anthu onse amene ankakhala m'nyumba ya Ziba, adasanduka atumiki a Mefiboseti. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mefiboseti anali ndi mwana wamngʼono wamwamuna wotchedwa Mika, ndipo onse a banja la Ziba anali antchito a Mefiboseti. |
Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzachita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu.
Chomwecho Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ake onse awiri.
ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.