2 Samueli 7:5 - Buku Lopatulika Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Kamuuze mtumiki wanga Davide kuti Ine Chauta ndikuti, Kani wayesa udzandimangira ndiwe nyumba yoti ndizikhalamo? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti: kodi ndiwe amene udzandimangira Ine nyumba yokhalamo? |
Ndipo mfumu inalamula iwo, natuta miyala yaikuluikulu ya mtengo wapatali, kuika maziko ake a nyumbayo ndi miyala yosemasema.
Kunena za nyumba ino ulikuimanga, ukamayenda iwe m'malemba anga, ndi kumachita maweruzo anga, ndi kumasunga malamulo anga onse kuyendamo, pamenepo Ine ndidzakhazikitsira iwe mau anga amene ndinauza Davide atate wako.
Koma Mulungu anati kwa ine, Sudzamangira dzina langa nyumba, popeza ndiwe munthu wa nkhondo wokhetsa mwazi.
Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?