Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 7:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 “Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti: kodi ndiwe amene udzandimangira Ine nyumba yokhalamo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 “Kamuuze mtumiki wanga Davide kuti Ine Chauta ndikuti, Kani wayesa udzandimangira ndiwe nyumba yoti ndizikhalamo?

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 7:5
11 Mawu Ofanana  

Usiku umenewo mawu a Yehova anafika kwa Natani ndipo anati,


Molamulidwa ndi mfumu, anakumba ndi kusema miyala ikuluikulu kwambiri yoti akamangire maziko a Nyumba ya Mulungu.


“Kunena za Nyumba imene ukumangayi, ngati iwe udzamvera malangizo anga ndi kutsatira mawu anga, ngati udzasunga malamulo anga ndi kuwachita, Ine ndidzakwaniritsa zonse zomwe ndinalonjeza Davide abambo ako.


“Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti, sudzandimangira ndiwe nyumba yokhalamo.’


Koma Mulungu anati kwa ine, “Usandimangire nyumba chifukwa ndiwe munthu wankhondo ndipo wakhala ukukhetsa magazi.”


Zolinga za mu mtima ndi za munthu, koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho.


Yehova akuti, “Kumwamba ndi mpando wanga waufumu ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga. Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire, ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa