Ndipo Hiramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba.
2 Samueli 7:1 - Buku Lopatulika Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwake, atampumulitsa Yehova pa adani ake onse omzungulira, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwake, atampumulitsa Yehova pa adani ake onse omzungulira, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi imene mfumu Davide anali atakhazikika m'nyumba mwake, Chauta adampumuza kwa adani ake onse omzungulira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mfumu itakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, Yehova atayipatsa mpumulo kwa adani ake onse woyizungulira, |
Ndipo Hiramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba.
monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israele; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.
Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipumulitsa ku mbali zonse; palibe wotsutsana nane, kapena choipa chondigwera.
Pamenepo iye anaitana Solomoni mwana wake, namlangiza ammangire Yehova Mulungu wa Israele nyumba.
Ndipo Davide anati kwa Solomoni mwana wake, Kunena za ine, kumtima kwanga kudati, ndilimangire dzina la Yehova Mulungu wanga nyumba.
Ndipo mfumu Davide anaima chilili, nati, Mundimvere ine, abale anga ndi anthu anga, ine kumtima kwanga ndinafuna kulimangira likasa la chipangano la Yehova, ndi popondapo mapazi a Mulungu wathu nyumba yopumulira, ndipo ndidakonzeratu za nyumbayi.
Ndipo anamanga mizinda yamalinga mu Yuda; pakuti dziko linachita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa.
Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu.
amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalamo Mulungu wa Yakobo.
Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaime munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m'manja mwao.
Ndipo atapita masiku ambiri, Yehova atapumulitsa Israele kwa adani ao onse akuwazungulira, ndipo Yoswa adakalamba nakhala wa zaka zambiri;