Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 7:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mfumu itakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, Yehova atayipatsa mpumulo kwa adani ake onse woyizungulira,

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwake, atampumulitsa Yehova pa adani ake onse omzungulira,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwake, atampumulitsa Yehova pa adani ake onse omzungulira,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Nthaŵi imene mfumu Davide anali atakhazikika m'nyumba mwake, Chauta adampumuza kwa adani ake onse omzungulira.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 7:1
19 Mawu Ofanana  

Tsono Hiramu mfumu ya Turo inatumiza amithenga ake kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndi amisiri a matabwa ndi amisiri a miyala, ndipo anamumangira Davide nyumba yaufumu.


Ndipo Mikala mwana wa Sauli sanakhalenso ndi mwana mpaka anamwalira.


monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzakupatsaninso mpumulo kwa adani anu onse. “ ‘Yehova akulengeza kwa iwe kuti Iye mwini adzakhazikitsa banja lako:


Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipatsa mtendere mbali zonse za dziko ndipo ndilibe mdani kapena chovuta chilichonse.


Tsono iye anayitana Solomoni mwana wake ndipo anamulamula kuti adzamangire nyumba Yehova Mulungu wa Israeli.


Davide anati kwa Solomoni, “Mwana wanga, ine ndinali ndi maganizo oti ndimangire nyumba Dzina la Yehova Mulungu wanga.


Mfumu Davide inayimirira ndipo inati: “Tamverani abale anga ndi anthu anga. Ine ndinali ndi maganizo omanga nyumba monga malo okhalamo Bokosi la Chipangano la Yehova, malo oyikapo mapazi a Mulungu wathu, ndipo ndinakonza ndondomeko yomangira nyumbayo.”


Asa anamanga mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda pakuti dziko linali pa mtendere. Panalibe amene anachita naye nkhondo mʼzaka zimenezo, pakuti Yehova anamupatsa mpumulo.


Ndipo ufumu wa Yehosafati unali pa mtendere pakuti Mulungu wake anamupatsa mpumulo ku mbali zonse.


mpaka nditamupezera malo Yehova, malo okhala a Wamphamvu wa Yakobo.”


Davide anati: Ine ndimakukondani Inu Yehova, mphamvu zanga.


Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Yehova, ngakhale adani ake amakhala naye mwa mtendere.


Munthu amene analandira ndalama 5,000 uja, anapita nthawi yomweyo nachita nazo malonda napindula 5,000 zina.


amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu ndipo anapempha kuti amʼmangire nyumba Mulungu wa Yakobo.


Yehova anawapatsa mtendere mʼdziko lonse monga momwe analonjezera makolo awo. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa adani awo amene anatha kuwagonjetsa chifukwa Yehova anapereka adani awo onse mʼmanja mwawo.


Panapita nthawi yayitali kuchokera pamene Yehova anakhazikitsa mtendere pakati pa Aisraeli ndi adani awo owazungulira. Nthawi imeneyi nʼkuti Yoswa atakalamba, ali ndi zaka zambiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa