Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, chifukwa cha kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu.
2 Samueli 6:8 - Buku Lopatulika Ndipo kudaipira Davide, chifukwa Yehova anachita chipasulo ndi Uza; natcha malowo Pereziuza, kufikira lero lino. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kudaipira Davide, chifukwa Yehova anachita chipasulo ndi Uza; natcha malowo Pereziuza, kufikira lero lino. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Davide adakhumudwa chifukwa chakuti Chauta adaakantha Uza. Ndipo mpaka pano malo amenewo amaŵatchula kuti Pereziuza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza. |
Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, chifukwa cha kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu.
Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine?
Pakuti, chifukwa cha kusalinyamula inu poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula, popeza sitinamfunafuna Iye monga mwa chiweruzo.
Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.