Ndipo Hiramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba.
2 Samueli 5:12 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova anamkhazikitsa mfumu ya Israele, ndi kuti anakulitsa ufumu wake chifukwa cha anthu ake Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova anamkhazikitsa mfumu ya Israele, ndi kuti anakulitsa ufumu wake chifukwa cha anthu ake Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Davide adazindikira kuti Chauta wamkhazikitsa kuti akhale mfumu yolamulira Aisraele, ndiponso kuti wakweza ufumu wake chifukwa cha Aisraele, anthu ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Davide anazindikira kuti Yehova wamukhazikitsa kukhala mfumu ya Israeli ndipo wakuza ufumu wake chifukwa cha anthu ake, Aisraeli. |
Ndipo Hiramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba.
Ndipo Davide anadzitengera akazi aang'ono ena ndi akazi a ulemu ena a ku Yerusalemu, atafikako kuchokera ku Hebroni; ndipo anambadwira Davide ana aamuna ndi aakazi.
Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.
Wolemekezeka Yehova Mulungu wanu amene anakondwera nanu, kukuikani pa mpando wachifumu wa Israele; popeza Yehova anakonda Israele nthawi yosatha, chifukwa chake anakulongani inu ufumu, kuti muchite chiweruzo ndi chilungamo.
Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova adamkhazikitsa mfumu ya Israele; pakuti ufumu wake unakwezekadi, chifukwa cha anthu ake Israele.
Ndipo Huramu mfumu ya Tiro anayankha ndi kulembera, natumiza kalatayo kwa Solomoni, ndi kuti, Powakonda anthu ake Yehova anakulongani mfumu yao.
Pakuti ukakhala chete konse tsopano lino, chithandizo ndi chipulumutso kwa Ayuda zidzafuma kwina; koma iwe ndi nyumba ya atate wako mudzaonongeka; ndipo kaya, kapena walowera ufumu chifukwa cha nyengo yonga iyi.
Koma ine, chinsinsi ichi sichinavumbulutsidwe kwa ine chifukwa cha nzeru ndili nayo yakuposa wina aliyense wamoyo, koma kuti kumasuliraku kudziwike kwa mfumu, ndi kuti mudziwe maganizo a mtima wanu.
Madzi adzayenda natuluka m'zotungira zake, ndi mbeu zake zidzakhala ku madzi ambiri, ndi mfumu yake idzamveka koposa Agagi, ndi ufumu wake udzamveketsa.