Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 7:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono banja lako pamodzi ndi ufumu wako ndidzazikhazikitsa mpaka muyaya pamaso panga. Ndithudi, ufumu wako udzakhazikika osatha konse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhala zamuyaya pamaso panga. Mpando wako waufumu udzakhazikika kwamuyaya!’ ”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 7:16
29 Mawu Ofanana  

Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.


Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu; naonetsera chifundo wodzozedwa wake, kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse.


Iye adzamangira dzina langa nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wake ku nthawi zonse.


Monga mwa mau onse awa ndi monga mwa masomphenya onse awa, momwemo Natani analankhula ndi Davide.


kuti Yehova akakhazikitse mau ake adanenawo za ine, kuti, Ngati ana ako akasunga bwino njira zao, kuyenda moona pamaso pa Ine ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, nditi sipadzakusowa mwamuna mmodzi pa mpando wachifumu wa Israele.


pamenepo Ine ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wako pa Israele nthawi yosatha, monga ndinalonjezana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wamwamuna pa mpando wachifumu wa Israele.


Pakuti ndidzatchinjiriza mzinda uno kuupulumutsa, chifukwa cha Ine mwini, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.


Koma Yehova sanafune kuononga Yuda, chifukwa cha Davide mtumiki wake monga adamuuza, kuti adzampatsa nyali ya kwa ana ake kosalekeza.


Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wakukhala pa mpando wachifumu wa Israele; pokhapo ngati ana ako asamalira njira yao, kuti ayende m'chilamulo changa, monga umo unayendera iwe pamaso panga.


Sawachotsera wolungama maso ake, koma pamodzi ndi mafumu pa mpando wao awakhazika chikhazikire, ndipo akwezeka.


Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ukhala nthawi zonse zomka muyaya. Ndodo yachifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.


Adzakuopani momwe likhalira dzuwa ndi mwezi, kufikira mibadwomibadwo.


Ndidzakhazika mbeu yako kunthawi yonse, ndipo ndidzamanga mpando wachifumu wako ku mibadwomibadwo.


Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.


Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.


pamenepo padzalowa pa zipata za mzinda uwu mafumu ndi akulu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera pa magaleta ndi akavalo, iwo, ndi akulu ao, anthu a Yuda, ndi okhala mu Yerusalemu; ndipo mzinda uwu udzakhala kunthawi zamuyaya.


Pakuti Yehova atero: Davide sadzasowa munthu wokhala pa mpando wachifumu wa nyumba ya Israele;


Ndipo adzakhala m'dziko ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga, limene anakhalamo makolo anu, ndipo adzakhala m'mwemo iwo, ndi ana ao, ndi zidzukulu zao kosatha; ndi Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wao kosatha.


Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzaonongeka kunthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse, nudzakhala chikhalire.


Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.


Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.


Pamenepo khamulo linayankha Iye, Tidamva ife m'chilamulo kuti Khristu akhala kunthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa Munthu amene ndani?


Koma ponena za Mwana, ati, Mpando wachifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi; ndipo ndodo yachifumu yoongoka ndiyo ndodo ya ufumu wanu.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka choipa masiku anu onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa