Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 3:38 - Buku Lopatulika

Ndipo mfumu inati kwa anyamata ake, Simudziwe kodi kuti kalonga ndi munthu womveka wagwa lero mu Israele?

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mfumu inati kwa anyamata ake, Simudziwa kodi kuti kalonga, ndi munthu womveka, wagwa lero m'Israele?

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo mfumu Davide adafunsa ankhondo ake kuti, “Kodi simukudziŵa kuti lero m'dziko la Israele mwagwa kalonga amene ali munthu wamkulu?

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo mfumu inati kwa ankhondo ake, “Kodi inu simukudziwa kuti lero mu Israeli mwagwa kalonga ndi munthu wamkulu?

Onani mutuwo



2 Samueli 3:38
7 Mawu Ofanana  

Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;


Ndipo Abinere anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? Natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisraele onse atsate inu.


Momwemo anthu onse ndi Aisraele onse anazindikira tsiku lija kuti sikunafumire kwa mfumu kupha Abinere mwana wa Nere.


Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo ana aamuna awa a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.


Akulu sindiwo eni nzeru, ndi okalamba sindiwo ozindikira chiweruzo.


Davide nati kwa Abinere, Sindiwe mwamuna weniweni kodi? Ndani mwa Aisraele anafanafana ndi iwe? Unalekeranji tsono kudikira mbuye wako, mfumuyo? Pakuti anafika wina kudzaononga mfumu, mbuye wako.