Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 26:15 - Buku Lopatulika

15 Davide nati kwa Abinere, Sindiwe mwamuna weniweni kodi? Ndani mwa Aisraele anafanafana ndi iwe? Unalekeranji tsono kudikira mbuye wako, mfumuyo? Pakuti anafika wina kudzaononga mfumu, mbuye wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Davide nati kwa Abinere, Sindiwe mwamuna weniweni kodi? Ndani mwa Aisraele anafanafana ndi iwe? Unalekeranji tsono kudikira mbuye wako, mfumuyo? Pakuti anafika wina kudzaononga mfumu, mbuye wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Davide adafunsa Abinere kuti, “Kodi sindiwe mwamuna? Ndani ali wofanafana nawe m'dziko la Israele? Nanga chifukwa chiyani sudamlonde mbuyako mfumu? Tsopano apa munthu wina anabwera kumeneko kuti adzaphe mbuyakoyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Davide anamufunsa Abineri kuti, “Kodi sindiwe mwamuna? Ndipo wofanana nawe ndani mu Israeli? Nʼchifukwa chiyani sunateteze mbuye wako mfumu? Munthu wina anabwera kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 26:15
5 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inati kwa anyamata ake, Simudziwe kodi kuti kalonga ndi munthu womveka wagwa lero mu Israele?


Pamenepo Daniele, dzina lake ndiye Belitesazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ake. Mfumu inayankha, niti, Belitesazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwake. Belitesazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwake kwa iwo akuutsana nanu.


Ndipo anadza kwa ophunzira, nawapeza iwo ali m'tulo, nanena kwa Petro, Nkutero kodi? Simungathe kuchezera ndi Ine mphindi imodzi?


ndipo Davide anaitana anthuwo, ndi Abinere mwana wa Nere, nati Suyankha kodi Abinere? Tsono Abinere anayankha, nati, Ndiwe yani amene uitana mfumuyo?


Ichi unachichita sichili chabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, chifukwa simunadikire mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi chikho cha madzi zinali kumutu kwake zili kuti?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa