1 Samueli 26:16 - Buku Lopatulika16 Ichi unachichita sichili chabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, chifukwa simunadikire mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi chikho cha madzi zinali kumutu kwake zili kuti? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ichi unachichita sichili chabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, chifukwa simunadikira mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi chikho cha madzi zinali kumutu kwake zili kuti? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Zimene wachitazi si zabwino ai. Pali Chauta wamoyo, nonsenu muyenera kuphedwa chifukwa simudalonde mbuye wanu, wodzozedwa wa Chauta. Uyang'ane kumene kuli mkondo wa mfumu ndi mtsuko wa madzi, zimene zinali kumutu kwake.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Chimene wachita iwe si chabwino. Pali Yehova wamoyo iwe ndi asilikali ako muyenera kufa chifukwa simunateteze mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Tayangʼanayangʼana. Uli kuti mkondo wa mfumu ndi botolo lamadzi zimene zinali kumutu kwa mfumu?” Onani mutuwo |