Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 3:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo Abinere anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? Natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisraele onse atsate inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo Abinere anatuma mithenga imnenere kwa Davide, nati, Dziko nla yani? Natinso, Mupangane nane pangano lanu, ndipo onani, ndidzagwirizana nanu ndi kukopa Aisraele onse atsate inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Tsono Abinere adatuma amithenga kwa Davide ku Hebroni kukamufunsa kuti, “Kodi dzikoli nlayani? Tipangane, ine ndidzakuthandizani kuti dziko la Israele likhale lanu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kenaka Abineri anatuma amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Kodi dzikoli ndi la yani? Uchite mgwirizano ndi ine ndipo ndidzakuthandiza kuti Aisraeli onse azikutsatira.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 3:12
15 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anakopa mitima ya anthu onse a Yuda, monga munthu mmodzi, natumiza iwo kwa mfumu, nati, Mubwere inu ndi anyamata anu onse.


Ndipo onani, Aisraele onse anafika kwa mfumu, nanena ndi mfumu, Abale athu anthu a Yuda anakuchotsani bwanji mwakuba, naolotsa mfumu ndi banja lake pa Yordani, ndi anthu onse a Davide pamodzi naye?


m'mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu.


Ndipo iye sanakhoze kuyankha Abinere mau amodzi chifukwa cha kumuopa iye.


Nati iye, Chabwino, ndidzapangana nawe; koma ndikuikira chinthu chimodzi, ndicho kuti, sudzaona nkhope yanga, koma utsogole wabwera naye Mikala mwana wamkazi wa Saulo, pamene ubwera kudzaona nkhope yanga.


Pomwepo Abinere anati kwa Davide, Ndidzanyamuka ndi kupita ndi kusonkhanitsira mfumu mbuye wanga Aisraele onse, kuti adzapangane nanu pangano, ndi kuti mukhale mfumu pa zonse mtima wanu uzikhumba. Chomwecho Davide analawirana ndi Abinere, namuka iye mumtendere.


Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Ndipo mfumu inati kwa anyamata ake, Simudziwe kodi kuti kalonga ndi munthu womveka wagwa lero mu Israele?


Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa