2 Samueli 3:36 - Buku Lopatulika Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthu onse anachisamalira, ndipo chinawakomera; zilizonse adazichita mfumu zidakomera anthu onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu onse adamvera zimenezo, ndipo zidaŵakomera. Zonse zimene ankachita mfumu zinkaŵakondwetsa anthu onse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu onse anadziwa zimenezi ndipo zinawakondweretsa ndithu. Zonse zimene mfumu inachita zinawakondweretsa. |
Abisalomu anachitira zotero Aisraele onse akudza kwa mfumu kuti aweruze mlandu wao; chomwecho Abisalomu anakopa mitima ya anthu a Israele.
Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide chakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa.
Momwemo anthu onse ndi Aisraele onse anazindikira tsiku lija kuti sikunafumire kwa mfumu kupha Abinere mwana wa Nere.
Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.
Ndipo anadabwa kwakukulukulu, nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.