Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga.
2 Samueli 3:34 - Buku Lopatulika Manja anu sanamangidwe, mapazi anu sanalongedwe m'zigologolo; monga munthu wakugwa ndi anthu oipa momwemo mudagwa inu. Ndipo anthu onse anamliranso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Manja anu sanamangidwe, mapazi anu sanalongedwe m'zigologolo; monga munthu wakugwa ndi anthu oipa momwemo mudagwa inu. Ndipo anthu onse anamliranso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Manja ako anali osamanga, mapazi ako anali osakulunga. Komabe wafa monga m'mene amafera munthu m'manja mwa anthu oipa mtima.” Anthu onse adaliranso, kumlira Abinere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Manja ako anali osamanga, mapazi ako anali osakulungidwa. Iwe wafa monga mmene amafera anthu pamaso pa anthu oyipa.” Ndipo anthu onse analiranso kulirira Abineri. |
Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga.
Ndipo mfumu inanenera Abinere nyimbo iyi ya maliro, niti, Kodi Abinere anayenera kufa ngati chitsiru?
Ndipo anthu onse anadza kudzadyetsa Davide chakudya kukali msana; koma Davide analumbira nati, Mulungu andilange naonjezepo, ngati ndilawa mkate kapena kanthu kena, lisanalowe dzuwa.
Iyi ndi nyimbo ya maliro adzalira nayo, ana aakazi a amitundu adzachita nayo maliro; adzalirira nayo Ejipito ndi aunyinji ake onse, ati Ambuye Yehova.
Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha panjira ya ku Sekemu; indedi achita choipitsitsa.
Pamenepo Afilisti anamgwira, namkolowola maso, natsika naye ku Gaza, nammanga ndi maunyolo amkuwa; namperetsa m'kaidi.