Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 6:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha panjira ya ku Sekemu; indedi achita choipitsitsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha pa njira ya ku Sekemu; indedi achita choipitsitsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Monga mbala zimalalira munthu, momwemonso ansembe amasonkhana kuti azipha anthu pa njira ya ku Sekemu. Zoonadi amachita zachifwamba zambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Monga momwe mbala zimadikirira anthu, magulu a ansembe amachitanso motero; iwo amapha anthu pa njira yopita ku Sekemu, kupalamula milandu yochititsa manyazi.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 6:9
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Abramu anapitirira m'dzikomo kufikira ku malo a Sekemu, kufikira ku mtengo wathundu wa ku More. Akanani anali m'dzikomo nthawi yomweyo.


Ndipo Yerobowamu anamanga Sekemu m'mapiri a Efuremu, nakhalamo, natulukamo, namanga Penuwele.


Pamenepo tinachoka ku mtsinje wa Ahava tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi woyamba, kunka ku Yerusalemu; ndipo dzanja la Mulungu wathu linakhala pa ife, ndi kutilanditsa m'dzanja la mdani ndi wolalira m'njira.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Chiwembu chaoneka mwa anthu a Yuda, ndi mwa anthu okhala mu Yerusalemu.


Pali chiwembu cha aneneri ake pakati pake, ngati mkango wobangula womwetula nyama, analusira miyoyo, alanda chuma ndi za mtengo wake, achulukitsa amasiye pakati pake.


Akalonga ake m'kati mwake akunga mimbulu yakumwetula nyama, kukhetsa mwazi, kuononga miyoyo, kuti aone phindu lonyenga.


Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anachita zamanyazi.


Motero ndidzakuleketsera choipa chako, ndi chigololo chako chochokera m'dziko la Ejipito; ndipo sudzazikwezeranso maso ako, kapena kukumbukiranso Ejipito.


Ndipo tsopano ndidzaonetsa manyazi ake pamaso pa omkonda, popandanso wakumlanditsa m'dzanja langa.


Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.


Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori.


Ndipo opandukawo analowadi m'zovunda; koma Ine ndine wakuwadzudzula onsewo.


M'mene ndichiritsa Israele, mphulupulu ya Efuremu ivumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti achita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala lilanda kubwalo.


Tamvanitu ichi, akulu a nyumba ya Yakobo inu, ndi oweruza a nyumba ya Israele inu, akuipidwa nacho chiweruzo, ndi kupotoza zoongoka zonse.


Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.


Akalonga ake m'kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.


Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:


Pamenepo ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa akulu, nanena, Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.


Ndipo m'mene adamva, anakweza mau kwa Mulungu ndi mtima umodzi, nati, Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili m'menemo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa