Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 3:34 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

34 Manja ako anali osamanga, mapazi ako anali osakulungidwa. Iwe wafa monga mmene amafera anthu pamaso pa anthu oyipa.” Ndipo anthu onse analiranso kulirira Abineri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

34 Manja anu sanamangidwe, mapazi anu sanalongedwe m'zigologolo; monga munthu wakugwa ndi anthu oipa momwemo mudagwa inu. Ndipo anthu onse anamliranso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

34 Manja anu sanamangidwe, mapazi anu sanalongedwe m'zigologolo; monga munthu wakugwa ndi anthu oipa momwemo mudagwa inu. Ndipo anthu onse anamliranso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

34 Manja ako anali osamanga, mapazi ako anali osakulunga. Komabe wafa monga m'mene amafera munthu m'manja mwa anthu oipa mtima.” Anthu onse adaliranso, kumlira Abinere.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 3:34
8 Mawu Ofanana  

Iwo analira maliro ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi mwana wake Yonatani, komanso chifukwa cha gulu la ankhondo la Yehova ndi nyumba ya Israeli, chifukwa anaphedwa ndi lupanga.


Mfumu inayimba nyimbo iyi ya maliro a Abineri: “Abineri nʼkufa motere monga mmene chimafera chitsiru.


Kenaka onse anabwera kwa Davide kumuwumiriza kuti adye kusanade. Koma Davide analumbira kuti, “Mulungu andilange ine, andilange kwambiri, ngati ndilawe buledi kapena chilichonse dzuwa lisanalowe!”


Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka ndipo amakapha osauka ndi amphawi; nthawi ya usiku iye amasanduka mbala.


“Mawu angawa adzakhala nyimbo ya maliro. Ana a akazi amitundu ya anthu adzayimba, kuyimbira Igupto ndi gulu lake lonse la nkhondo, akutero Ambuye Yehova.”


Monga momwe mbala zimadikirira anthu, magulu a ansembe amachitanso motero; iwo amapha anthu pa njira yopita ku Sekemu, kupalamula milandu yochititsa manyazi.


Afilisti anamugwira ndipo anamukolowola maso. Kenaka anapita naye ku Gaza atamumanga ndi maunyolo achitsulo. Kumeneko anakhala wa pamphero mu ndende.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa