Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga.
2 Samueli 3:32 - Buku Lopatulika Ndipo anaika Abinere ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ake nilira ku manda a Abinere, nalira anthu onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anaika Abinere ku Hebroni; ndi mfumu inakweza mau ake nilira ku manda a Abinere, nalira anthu onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adakamuika Abinere ku Hebroni. Ndiye mfumu idalira mokweza mau ku manda a Abinere. Nawonso anthu onse adalira kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anamuyika Abineri mʼmanda ku Hebroni ndipo mfumu inalira mokweza pa manda a Abineri. Ndipo anthu onse analiranso. |
Nabuma, nalira misozi, nasala kudya kufikira madzulo, chifukwa cha Saulo ndi mwana wake Yonatani, ndi anthu a Yehova, ndi banja la Israele, chifukwa adagwa ndi lupanga.
Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!
Ndipo Davide analamulira anyamata ake, iwo nawapha, nawapachika m'mbali mwa thamanda ku Hebroni atawadula manja ndi mapazi ao. Koma mutu wa Isiboseti anautenga nauika m'manda a Abinere ku Hebroni.
ichinso ndi mphulupulu yoyenera oweruza kunena mlandu wake; pakuti ndikadakana Mulungu ali m'mwamba.
Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.