M'malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako, udzawaika akhale mafumu m'dziko lonse lapansi.
2 Samueli 24:23 - Buku Lopatulika zonsezi, mfumu, Arauna akupatsani mfumu. Ndipo Arauna anati kwa mfumu, Yehova Mulungu wanu akulandireni. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 zonsezi, mfumu, Arauna akupatsani mfumu. Ndipo Arauna anati kwa mfumu, Yehova Mulungu wanu akulandireni. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zonsezi Arauna adazipereka kwa mfumu, ndipo adapitiriza nati, “Chauta Mulungu wanu, alandire nsembe zanuzo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mfumu, Arauna akupereka zonsezi kwa inu mfumu.” Arauna anatinso kwa iye, “Yehova Mulungu wanu akuvomerezeni.” |
M'malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako, udzawaika akhale mafumu m'dziko lonse lapansi.
Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebayoti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa paguwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.
Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito.
inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.