Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 24:20 - Buku Lopatulika

Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ake alikubwera kwa iye; natuluka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yake pansi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Arauna anayang'ana naona mfumuyo ndi anyamata ake alikubwera kwa iye; natuluka Arauna naweramira pamaso pa mfumu nkhope yake pansi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo Arauna atapenya chakunsi, adaona mfumu ikudza kwa iye pamodzi ndi atumiki ake. Pomwepo Araunayo adapita kukalambira mfumu choŵerama pansi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Arauna atayangʼana ndi kuona mfumu ndi anthu ake akubwera kumene kunali iye, iyeyo anatuluka ndi kuwerama pamaso pa mfumu mpaka nkhope yake kugunda pansi.

Onani mutuwo



2 Samueli 24:20
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anatukula maso ake, nayang'ana, taonani, anthu atatu anaima pandunji pake; pamene anaona iwo, anawathamangira kuchoka ku khomo la hema kukakomana nao, nawerama pansi, nati,


pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.


Ndipo Davide anakwerako monga mwa kunena kwa Gadi, monga adalamulira Yehova.


Arauna nati, Mbuye wanga mfumu, mwadzeranji kwa mnyamata wanu? Ndipo Davide, anati, Kugula dwale lako ili, kuti ndimangirepo Yehova guwa la nsembe, kuti mliriwo ulekeke kwa anthu.


Ndipo iye anamlambira, nati, Mnyamata wanu ndani, kuti mulikupenya galu wakufa monga ine.


Potero anagwa nkhope yake pansi, nadziweramira pansi, nanena naye, Mwandikomera mtima chifukwa ninji kuti mundisamalira ine, popeza ndine mlendo?