Ndipo anafika pa dwale la Atadi, lili tsidya lija la Yordani, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi.
2 Samueli 24:18 - Buku Lopatulika Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Myebusi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Myebusi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsiku limenelo Gadi adafika kwa Davide namuuza kuti, “Mupite mukamangire Chauta guwa pa malo opunthira tirigu a Arauna Myebusi uja.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku limenelo Gadi anapita kwa Davide ndi kukanena kuti, “Pitani kamangeni guwa lansembe la Yehova pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.” |
Ndipo anafika pa dwale la Atadi, lili tsidya lija la Yordani, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi.
Ndipo pouka Davide m'mawa mau a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlauli wa Davide, kuti,
Pamenepo Solomoni anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, m'phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wake pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi.
Ndipo ndidzachotsa mwazi wake m'kamwa mwake, ndi zonyansa zake pakati pa mano ake; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkulu wa fuko mu Yuda, ndi Ekeroni ngati Myebusi.