Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 9:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo ndidzachotsa mwazi wake m'kamwa mwake, ndi zonyansa zake pakati pa mano ake; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkulu wa fuko mu Yuda, ndi Ekeroni ngati Myebusi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo ndidzachotsa mwazi wake m'kamwa mwake, ndi zonyansa zake pakati pa mano ake; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati mkulu wa fuko m'Yuda, ndi Ekeroni ngati Myebusi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Anthu ake sadzadyanso nyama yamagazi, kapena nyama yoletsedwa iliyonse. Otsala onse adzakhala anthu anga, adzasanduka ngati fuko la ku Yuda. Nawonso Aekeroni adzakhala ngati Ayebusi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndidzachotsa nyama ya magazi mʼkamwa mwawo, chakudya choletsedwa mʼmano mwawo. Amene atsala adzakhala anthu a Mulungu wathu, adzasanduka atsogoleri mu Yuda, ndipo Ekroni adzakhala ngati Ayebusi.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 9:7
21 Mawu Ofanana  

ndi Ayebusi, ndi Aamori, ndi Agirigasi,


Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka choipachi; nati kwa mthenga wakuononga, Chakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi.


Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.


Thyolani mano ao m'kamwa mwao, Mulungu, zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova.


amene akhala pakati pa manda, ndi kugona m'malo am'tseri; amene adya nyama ya nkhumba, ndi msuzi wa zinthu zonyansa uli m'mbale zao;


Koma ndidzabwezanso undende wa Mowabu masiku akumaliza, ati Yehova. Ziweruzo za Mowabu ndi zomwezi.


Koma padzaoneka masiku akutsiriza, kuti ndidzabwezanso undende wa Elamu, ati Yehova.


Koma pambuyo pake ndidzabwezanso undende wa ana a Amoni, ati Yehova.


Atero Yehova, Monga mbusa alanditsa m'kamwa mwa mkango miyendo iwiri, kapena kansonga ka khutu, momwemo adzalanditsidwa ana a Israele okhala pansi mu Samariya, m'ngodya ya guwa logonapo, ndi pa mitsamiro ya kama.


Atero Yehova wa makamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.


Ndi mtundu wa anthu osokonezeka udzakhala mu Asidodi, ndipo ndidzaononga kudzikuza kwa Afilisti.


Ndipo ndidzamangira nyumba yanga misasa, kuiletsera nkhondo, asapitepo munthu kapena kubweranso; ndipo wakuwasautsa sadzapitanso pakati pao; pakuti tsopano ndapenya ndi maso anga.


Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa