Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Mbiri 3:1 - Buku Lopatulika

1 Pamenepo Solomoni anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, m'phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wake pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamenepo Solomoni anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, m'phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wake pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsono Solomoni adayambapo kumanga Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu pa phiri la Moriya, pamene Chauta adaaonekera Davide bambo wake, pa malo omwe Davide adaaloza, pa bwalo lopunthira tirigu la Orinani Myebusi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Pamenepo Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu pa Phiri la Moriya, pamene Yehova anaonekera Davide abambo ake. Panali pabwalo lopunthirapo tirigu la Arauna Myebusi, malo amene anapereka Davide.

Onani mutuwo Koperani




2 Mbiri 3:1
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anatcha dzina lake la malowo Yehova-Yire: monga ati lero lomwe, M'phiri la Yehova chidzaoneka.


Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isaki, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.


Ndipo pamene mthenga anatambasulira dzanja lake ku Yerusalemu kuuononga, choipacho chinachititsa Yehova chisoni, Iye nauza mthenga wakuononga anthuwo, kuti, Kwafikira tsopano, bweza dzanja lako. Ndipo mthenga wa Yehova anali pa dwale la Arauna Myebusi.


Pamenepo mthenga wa Yehova analamula Gadi kuti anene ndi Davide, akwere Davideyo kuutsira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani Myebusi.


Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israele.


ndi Yohanani anabala Azariya (ndiye amene anachita ntchito ya nsembe m'nyumba anaimanga Solomoni mu Yerusalemu),


Nayamba kumanga tsiku lachiwiri la mwezi wachiwiri, chaka chachinai cha ufumu wake.


Koma Solomoni anammangira nyumba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa