Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.
2 Samueli 22:47 - Buku Lopatulika Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa; ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la chipulumutso changa; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa; ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la chipulumutso changa; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Chauta ndiwamoyo. Litamandike thanthwe langa, alemekezeke Mulungu wanga, thanthwe londipulumutsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa. Akuzike Mulungu, Thanthwe, Mpulumutsi wanga! |
Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.
Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga, Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.