Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala.
2 Samueli 22:34 - Buku Lopatulika Iye asandutsa mapazi ake akunga mapazi a mbawala; nandiika pa misanje yanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iye asandutsa mapazi ake akunga mapazi a mbawala; nandiika pa misanje yanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amalimbitsa mapazi anga ngati a mbaŵala, ndipo amandisunga bwino ku mapiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi; Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri. |
Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala.
Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa: Atero Davide mwana wa Yese, atero munthu wokwezedwa, ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele.
iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.
pomwepo udzakondwa mwa Yehova; ndipo Ine ndidzakuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi; ndipo ndidzakudyetsa cholowa cha kholo lako Yakobo; pakuti pakamwa pa Yehova pananenapo.
Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga, asanduliza mapazi anga ngati a mbawala, nadzandipondetsa pa misanje yanga.
Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi, ndipo anadya zipatso za m'minda; namyamwitsa uchi wa m'thanthwe, ndi mafuta m'mwala wansangalabwe;
Nsapato zako zikhale za chitsulo ndi mkuwa; ndipo monga masiku ako momwemo mphamvu yako.