Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.
2 Samueli 22:30 - Buku Lopatulika Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu; ndi Mulungu wanga ndilumphira linga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu; ndi Mulungu wanga ndilumphira linga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndi chithandizo chanu ndingathe kugonjetsa gulu la ankhondo. Ndi chithangato chanu, Inu Mulungu, ndingathe kupambana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo, ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu. |
Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.
Ndipo mfumu ndi anthu ake anamuka ku Yerusalemu kuyambana nao Ayebusi, nzika za dziko; ndiwo ananena kwa Davide ndi kuti, Sudzalowa muno, koma akhungu ndi opunduka adzakupirikitsa; ndiko kunena kuti, Davide sangathe kulowa muno.