Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu.
2 Samueli 22:19 - Buku Lopatulika Anandifikira ine tsiku la tsoka langa; koma Yehova anali mchirikizo wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Anandifikira ine tsiku la tsoka langa; koma Yehova anali mchirikizo wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaniwo adandithira nkhondo pamene ndinali m'mavuto, koma Chauta adandichirikiza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto, koma Yehova anali thandizo langa. |
Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu.
Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muimbe, inu amene mukhala m'fumbi; chifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzatulutsa mizimu.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.