Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 21:4 - Buku Lopatulika

Ndipo Agibiyoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golide wa Saulo kapena nyumba yake; ndiponso sitifuna kupha munthu aliyense wa mu Israele. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakuchitirani.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Agibiyoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golide wa Saulo kapena nyumba yake; ndiponso sitifuna kupha munthu aliyense wa m'Israele. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakuchitirani.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Agibiyoniwo adauza Davide kuti, “Mlandu umene ulipo pakati pa ife ndi Saulo kapena banja lake, si woti nkulipira ndi golide kapena siliva, ndiponso sikuti kapena ife tikufuna kulipira pakupha wina aliyense m'dziko la Israele ai.” Apo Davide adafunsanso kuti, “Nanga tsono mukuti ndikuchitireni chiyani?”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Agibiyoni anamuyankha kuti, “Ife tilibe ufulu woti nʼkulamula Sauli ndi banja lake kuti atipatse siliva kapena golide, tilibenso ufulu woti nʼkupha wina aliyense mu Israeli.” Davide anafunsa, “Mukufuna ine ndikuchitireni chiyani?”

Onani mutuwo



2 Samueli 21:4
5 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anati, Ndikupatsa iwe bwanji? Ndipo Yakobo anati, Usandipatse ine kanthu; ukandichitira ine chotero, ine ndidzadyetsanso ndi kusunganso ziweto zako.


Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, napalamula imfa; koma aziphedwa ndithu.


Musamalandira dipo lakuombola iye amene adathawira kumzinda wake wopulumukirako, kuti abwerenso kukhala m'dziko, kufikira atafa mkulu wa ansembe.