Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 35:32 - Buku Lopatulika

32 Musamalandira dipo lakuombola iye amene adathawira kumzinda wake wopulumukirako, kuti abwerenso kukhala m'dziko, kufikira atafa mkulu wa ansembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Musamalandira dipo lakuombola iye amene adathawira kumudzi wake wopulumukirako, kuti abwerenso kukhala m'dziko, kufikira atafa mkulu wa ansembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Ndipo musalandire dipo loombolera munthu amene ali mu mzinda wake wothaŵirako kuti abwerere ndi kukakhala ku dziko lake, mkulu wa ansembeyo asanamwalire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 “ ‘Simuyeneranso kulandira dipo kwa munthu amene wathawira ku mzinda wopulumikirako kuti wothawayo abwerere kwawo, pokhapokha ngati mkulu wa ansembe wamwalira.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 35:32
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Agibiyoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golide wa Saulo kapena nyumba yake; ndiponso sitifuna kupha munthu aliyense wa mu Israele. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakuchitirani.


Musamalandira dipo lakuombola moyo wa iye adapha munthu, napalamula imfa; koma aziphedwa ndithu.


Ndipo musamaipsa dziko muli m'mwemo; popeza mwazi uipsa dziko; pakuti kulibe kutetezera dziko chifukwa cha mwazi anaukhetsa m'mwemo, koma ndi mwazi wa iye anaukhetsa ndiwo.


Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.


Sindichiyesa chopanda pake chisomo cha Mulungu; pakuti ngati chilungamo chili mwa lamulo, Khristu adafa chabe.


Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.


Ndipo aimba nyimbo yatsopano, ndi kunena, Muyenera kulandira bukulo, ndi kumasula zizindikiro zake; chifukwa mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa