Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 21:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Agibiyoni anamuyankha kuti, “Ife tilibe ufulu woti nʼkulamula Sauli ndi banja lake kuti atipatse siliva kapena golide, tilibenso ufulu woti nʼkupha wina aliyense mu Israeli.” Davide anafunsa, “Mukufuna ine ndikuchitireni chiyani?”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo Agibiyoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golide wa Saulo kapena nyumba yake; ndiponso sitifuna kupha munthu aliyense wa mu Israele. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakuchitirani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Agibiyoni ananena naye, Sitifuna siliva kapena golide wa Saulo kapena nyumba yake; ndiponso sitifuna kupha munthu aliyense wa m'Israele. Nati iye, Monga inu mudzanena, momwemo ndidzakuchitirani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Agibiyoniwo adauza Davide kuti, “Mlandu umene ulipo pakati pa ife ndi Saulo kapena banja lake, si woti nkulipira ndi golide kapena siliva, ndiponso sikuti kapena ife tikufuna kulipira pakupha wina aliyense m'dziko la Israele ai.” Apo Davide adafunsanso kuti, “Nanga tsono mukuti ndikuchitireni chiyani?”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 21:4
5 Mawu Ofanana  

Labani anafunsa, “Ndikupatse chiyani?” Yakobo anayankha, “Musandipatse kanthu. Koma mungondichitira izi ndipo ndidzapitiriza kusamalira nkhosa zanu ndi kuziyangʼanira:


“ ‘Osalola kulandira dipo lowombolera munthu wakupha yemwe ayenera kuphedwa. Wakupha ayenera kuphedwa.


“ ‘Simuyeneranso kulandira dipo kwa munthu amene wathawira ku mzinda wopulumikirako kuti wothawayo abwerere kwawo, pokhapokha ngati mkulu wa ansembe wamwalira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa