Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.
2 Samueli 20:4 - Buku Lopatulika Pamenepo mfumu inati kwa Amasa, Undiitanire anthu a Yuda asonkhane asanapite masiku atatu, nukhale pano iwenso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo mfumu inati kwa Amasa, Undiitanire anthu a Yuda asonkhane asanapite masiku atatu, nukhale pano iwenso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mfumu idauza Amasa kuti, “Itanire anthu onse a ku Yuda, abwere kuno pasanapite masiku atatu, ndipo iweyo udzakhalepo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka mfumu inati kwa Amasa, “Itanitsa ankhondo a Yuda kuti abwere kwa ine pasanathe masiku atatu, ndipo iwe udzakhale nawo.” |
Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.
Ndipo munene ndi Amasa, Suli fupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala chikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yowabu.
Ndipo iye anakopa mitima ya anthu onse a Yuda, monga munthu mmodzi, natumiza iwo kwa mfumu, nati, Mubwere inu ndi anyamata anu onse.