2 Samueli 17:25 - Buku Lopatulika25 Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Abisalomu adaaika Amasa kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo m'malo mwa Yowabu. Amasa anali mwana wa munthu wina dzina lake Yetere Mwismaele, amene adaakwatira Abigala, mwana wa Nahasi, mlongo wa Zeruya amake a Yowabu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Abisalomu anasankha Amasa kukhala mkulu wa ankhondo mʼmalo mwa Yowabu. Amasa anali mwana wa munthu wotchedwa Itira Mwisraeli amene anakwatira Abigayeli mwana wa Nahasi mlongo wake wa Zeruya, amayi ake a Yowabu. Onani mutuwo |
Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.
Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m'chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake.