Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti iyo Nena.
2 Samueli 20:17 - Buku Lopatulika Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yowabu kodi? Iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndilikumva. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayandikira kwa mkaziyo; ndi mkaziyo anati, Ndinu Yowabu kodi? Iye nayankha, Ndine amene. Pamenepo ananena naye, Imvani mau a mdzakazi wanu. Iye nayankha, Ndilikumva. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yowabuyo adadza pafupi ndi mkaziyo, ndipo mkazi uja adamufunsa kuti, “Kodi inu ndinu aYowabu?” Yowabu adayankha kuti, “Ndine amene.” Mkaziyo adamuuza kuti, “Pepani bambo, mumvere mau anga.” Apo Yowabu adayankha kuti, “Inde, ndilikumva!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yowabu anayandikira kumene kunali mayiyo, ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndinu Yowabu?” Iye anayankha kuti, “Ndine.” Mayiyo anati, “Tamverani zimene mtumiki wanu akuti anene.” Yowabu anayankha kuti, “Ndikumvetsera.” |
Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti iyo Nena.
Pamenepo mkazi wanzeru wa m'mzindamo anafuula, kuti, Imvani, imvani; munene kwa Yowabu, Bwerani pafupi kuno kuti ndilankhule nanu.
Ndipo iye analankhula, nati, Kale adanena kuti, Zoonadi adzapempha uphungu ku Abele; ndipo potero mlandu udatha.
Ndipo atagwadira pa mapazi ake anati, Pa ine, mbuye wanga, pa ine pakhale uchimowo; ndipo mulole mdzakazi wanu alankhule m'makutu anu, nimumvere mau a mdzakazi wanu.