Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 20:11 - Buku Lopatulika

Ndipo mnyamata wina wa Yowabu anaima pali iye, nati, Wovomereza Yowabu, ndi iye amene ali wake wa Davide, atsate Yowabu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo mnyamata wina wa Yowabu anaima pali iye, nati, Wovomereza Yowabu, ndi iye amene ali wake wa Davide, atsate Yowabu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Wina mwa ankhondo a Yowabu adakaimirira pambali pa mtembo wa Amasa, nati, “Aliyense wokhumba Yowabu ndi Davide, mlekeni atsate Yowabuyo.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mmodzi mwa ankhondo a Yowabu anakayimirira pafupi ndi mtembo wa Amasa ndipo anati, “Aliyense amene amakonda Yowabu ndi aliyense amene ali wa Davide, atsatire Yowabu!”

Onani mutuwo



2 Samueli 20:11
6 Mawu Ofanana  

Ndipo Amasa analikukunkhulira m'mwazi wake pakati pa mseu. Ndipo pamene munthuyo anaona kuti anthu onse anaima, iye ananyamula Amasa namchotsa pamseu kunka naye kuthengo, namfunda ndi chovala, pamene anaona kuti anaima munthu yense wakufika pali iye.


Atamchotsa iye mumseu, anthu onse anapitirira kumtsata Yowabu kukalondola Sheba mwana wa Bikiri.


Mlanduwo suli wotere ai, koma munthu wa ku dziko lamapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri, anakweza dzanja lake pa mfumu Davide; mpereke iye yekha ndipo ndidzachoka mumzinda muno. Ndipo mkaziyo anati kwa Yowabu, Onani tidzakuponyerani mutu wake kutumphitsa linga.


Pamenepo mfumu inati kwa Amasa, Undiitanire anthu a Yuda asonkhane asanapite masiku atatu, nukhale pano iwenso.


Koma anakweza maso ake kuzenera, nati, Ali ndi ine ndani? Ndani? Nampenyererako adindo awiri kapena atatu.