2 Samueli 20:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo Amasa analikukunkhulira m'mwazi wake pakati pa mseu. Ndipo pamene munthuyo anaona kuti anthu onse anaima, iye ananyamula Amasa namchotsa pamseu kunka naye kuthengo, namfunda ndi chovala, pamene anaona kuti anaima munthu yense wakufika pali iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo Amasa analikukunkhulira m'mwazi wake pakati pa mseu. Ndipo pamene munthuyo anaona kuti anthu onse anaima, iye ananyamula Amasa namchotsa pamseu kunka naye kuthengo, namfunda ndi chovala, pamene anaona kuti anaima munthu yense wakufika pali iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Monsemo nkuti Amasa atagona pa mseu ndi kuvimvinizika m'magazi ake. Ndipo aliyense amene ankabwera, ankati akamuona, nkuima. Tsono munthu wa Yowabu uja ataona kuti anthu akuima, adanyamula Amasa uja, kumchotsa mumseumo, nakamuika ku thengo, nkumfunditsa chovala. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Amasa anagona pakati pa msewu atasamba magazi ake, ndipo munthuyo anaona kuti asilikali onse amayima pamenepo. Atazindikira kuti aliyense amene ankafika pamene panali Amasa amayima, iye anamuchotsa mu msewu ndi kumukokera mʼmunda ndipo anamuphimba ndi nsalu. Onani mutuwo |