wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri;
2 Samueli 2:2 - Buku Lopatulika Chomwecho Davide anakwera kunka kumeneko pamodzi ndi akazi ake awiri, ndiwo Ahinowamu Myezireele, ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho Davide anakwera kunka kumeneko pamodzi ndi akazi ake awiri, ndiwo Ahinowamu Myezireele, ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Davide adapita kumeneko pamodzi ndi akazi ake aŵiri aja, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Davide anapita kumeneko ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimeli. |
wachiwiri Kiliyabu, wa Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele; ndi wachitatu Abisalomu mwana wa Maaka mwana wamkazi wa Talimai mfumu ya ku Gesuri;
Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ake, munthu yense ndi a pabanja pake, inde Davide ndi akazi ake awiri, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile wa ku Karimele, mkazi wa Nabala.
Ndipo akazi awiri a Davide anatengedwa ukapolo, Ahinowamu wa ku Yezireele ndi Abigaile mkazi wa Nabala wa ku Karimele.