2 Samueli 2:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mizinda wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mudzi wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Pambuyo pake, Davide adafunsa Chauta kuti, “Kodi ndipite kukakhazikika ku mzinda wina uliwonse wa ku Yuda?” Chauta adamuuza kuti, “Inde, pita.” Apo Davide adafunsa kuti, “Tsono ndipite kuti?” Chauta adati, “Pita ku Hebroni.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Patapita nthawi, Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ku umodzi mwa mizinda ya Yuda?” Yehova anayankha kuti, “Pita.” Davide anafunsanso kuti, “Kodi ndipite kuti?” Yehova anayankha kuti, “Ku Hebroni.” Onani mutuwo |