Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 2:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Patapita nthawi, Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ku umodzi mwa mizinda ya Yuda?” Yehova anayankha kuti, “Pita.” Davide anafunsanso kuti, “Kodi ndipite kuti?” Yehova anayankha kuti, “Ku Hebroni.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mizinda wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mudzi wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pambuyo pake, Davide adafunsa Chauta kuti, “Kodi ndipite kukakhazikika ku mzinda wina uliwonse wa ku Yuda?” Chauta adamuuza kuti, “Inde, pita.” Apo Davide adafunsa kuti, “Tsono ndipite kuti?” Chauta adati, “Pita ku Hebroni.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 2:1
26 Mawu Ofanana  

Choncho Abramu anasamutsa tenti yake napita kukakhala pafupi ndi mitengo ikuluikulu ija ya thundu ya ku Mamre ku Hebroni, kumene anamangira Yehova guwa lansembe.


Pamene Yakobo anawaona anati, “Ili ndi gulu la Mulungu.” Choncho anawatcha malowo Mahanaimu.


Patapita zaka zinayi Abisalomu anati kwa mfumu, “Loleni ndipite ku Hebroni kuti ndikakwaniritse lonjezo limene ndinachita kwa Yehova.


Davide anakhala mfumu ku Hebroni akulamulira fuko la Yuda, kwa zaka zisanu ndi chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi.


Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka ndithu mʼmanja mwako.”


Davide anafunsa Yehova ndipo Yehovayo anayankha kuti, “Usapite molunjika koma uzungulire kumbuyo kwawo ndipo ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku.


Iyeyo nʼkuti atalamulira Israeli kwa zaka makumi anayi. Ku Hebroni analamulira zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33.


Iwo anapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu matani 170 a golide, matani 340 a siliva, matani 620 a mkuwa ndi matani 3,400 a chitsulo.


Zora, Ayaloni ndi Hebroni. Iyi ndiye inali mizinda yotetezedwa ya Yuda ndi Benjamini.


Lolani kuti mmawa ubweretse mawu achikondi chanu chosasinthika, pakuti ine ndimadalira Inu. Mundisonyeze njira yoti ndiyendemo, pakuti kwa Inu nditukulira moyo wanga.


Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova, ichi ndi chimene ndidzachifunafuna: kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova, ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.


“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzalolanso Aisraeli kuti andipemphe zoti ndiwachitire: Ndidzachulukitsa anthu awo ngati nkhosa.


Anapita kudzera ku Negevi ndi kukafika ku Hebroni, kumene Ahimani, Sesai ndi Talimai, ana a Anaki ankakhala. (Anamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri asanamange Zowani ku Igupto).


Ayime pamaso pa wansembe Eliezara, amene adzamudziwitse zimene Yehova akufuna pogwiritsa ntchito Urimu. Iye akalamula, Aisraeli onse azituluka ndipo akalamulanso, Aisraeliwo azibwereranso.”


Potsata lamulo la Yehova, Yoswa anapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune gawo lina la dziko la Yuda dera la Kiriati Ariba, limene ndi Hebroni. (Ariba anali gogo wa Aanaki).


Atamwalira Yoswa Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Ndani mwa ife ayambe nkhondo yomenyana ndi Akanaani?”


Tsono anthu anafunsanso kwa Yehova kuti, “Kodi munthuyu wabwera kale kuno?” Ndipo Yehova anayankha kuti, “Inde wabisala pakati pa katundu.”


anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ndikamenyane nawo Afilistiwa?” Yehova anamuyankha kuti, “Pita, kamenyane nawo Afilisti ndi kupulumutsa mzinda wa Keila.”


Davide anafunsanso Yehova, ndipo Yehova anamuyankha kuti, “Pita ku Keila pakuti ndapereka Afilisti mʼdzanja lako.”


Hebroni pamodzi ndi onse a kumalo kumene Davide ndi anthu ake anakhala akuyendayendako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa