Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere kunyumba yake.
2 Samueli 19:31 - Buku Lopatulika Ndipo Barizilai, Mgiliyadi anatsika kuchokera ku Rogelimu; nayambuka pa Yordani ndi mfumu, kuti akamuolotse pa Yordani. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Barizilai, Mgiliyadi anatsika kuchokera ku Rogelimu; nayambuka pa Yordani ndi mfumu, kuti akamuolotse pa Yordani. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Barizilai Mgiliyadi adafika kuchokera ku Rogelimu. Adapita ndi mfumu mpaka ku Yordani kuti akaiperekeze pooloka Yordani. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Barizilai Mgiliyadi anabweranso kuchokera ku Rogelimu kudzawoloka Yorodani ndi mfumu ndi kumuperekeza kuchokera kumeneko. |
Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere kunyumba yake.
Koma uchitire zokoma ana aamuna aja a Barizilai wa ku Giliyadi, akhale pakati pa akudyera pa gome lako, popeza momwemo amenewo anandiyandikira muja ndinalikuthawa Abisalomu mbale wako.
Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa dzina lao.
Ndi a ansembe: ana a Hobaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa ndi dzina lao.